Deuteronomy 32:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adaŵamwetsa chambiko wochokera ku ng'ombe ndiponso mkaka wankhosa, adaŵadyetsa nkhosa ndi mbuzi zonenepa, ndiponso nkhosa zamphongo zabwino za ku Basani, pamodzi ndi tirigu wabwino ndi vinyo wokoma.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
mafuta a mkaka wang'ombe, ndi mkaka wankhosa, ndi mafuta a anaankhosa, ndi nkhosa zamphongo za mtundu wa ku Basani, ndi atonde, ndi impso zonenepa zatirigu; ndipo munamwa vinyo, mwazi wamphesa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
pamodzi ndi chambiko ndi mkaka wochokera ku ngʼombe ndi nkhosa, ndiponso ana ankhosa onenepa ndi mbuzi, pamodzinso ndi nkhosa zazimuna zabwino za ku Basani ndiponso tirigu wabwino kwambiri. Munamwa vinyo wa thovu lofiira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mafuta a mkaka wang'ombe, ndi mkaka wankhosa, Ndi mafuta a ana a nkhosa, Ndi nkhosa zamphongo za mtundu wa ku Basana, ndi atonde, Ndi imso zonenepa zatirigu; Ndipo munamwa vinyo, mwazi wamphesa,