Deuteronomy 32:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yesuluni, anthu ake a Chauta adakulupala, koma iwowo adamuukira, adanenepa ndi kukula thupi, ndipo adakhuta zedi, kenaka adasiya Mulungu Mlengi wao, nanyoza mtetezi ndi mpulumutsi wao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Yesuruni anasanduka wonenepa, natazira; wasanduka wonenepa, wakula, wakuta ndi mafuta; pamenepo anasiya Mulungu amene anamlenga, napeputsa thanthwe la chipulumutso chake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yesuruni ananenepa ndi kuyamba kuwukira; atakhuta, ananenepa ndi kukula thupi. Anasiya Mulungu amene anamulenga ndipo anakana Thanthwe ndi Mpulumutsi wake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma Yesuruni anasanduka wonenepa, natazira; Wasanduka wonenepa, wakula, wakuta ndi mafuta; Pamenepo anasiya Mulungu amene anamlenga, Napeputsa thanthwe la cipulumutso cace.