Deuteronomy 32:20 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iye adati, “Ndidzaŵafulatira, ndidzaona chomwe chidzaŵachitikire, chifukwa anthu ameneŵa ngonyenga, ndi ana osakhulupirika.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Iye anati, Ndidzawabisira nkhope yanga, ndidzaona kutsiriza kwao; popeza iwo ndiwo mbadwo wopulukira, ana osakhulupirika iwo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anati, “Ndidzawabisira nkhope yanga, ndi kuona kuti mathero awo adzakhala otani; pakuti ndi mʼbado wopotoka, ana amene ndi osakhulupirika.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo iye anati, Ndidzawabisira nkhope yanga, Ndidzaona kutsiriza kwao; Popeza iwo ndiwo mbadwo wopulukira, Ana osakhulupirika iwo.