Deuteronomy 32:21 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Milungu yao yabodza ndachita nayo nsanje, mafano ao andikwiyitsa nawo. Inenso ndidzaŵachititsa nsanje pakusamalira mtundu wina wachabechabe, ndipo ndidzaŵapsetsa mtima pakukondera fuko lina lopanda pake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Anautsa nsanje yanga ndi chinthu chosati Mulungu; anautsa mkwiyo wanga ndi zopanda pake zao. Ndidzautsa nsanje yao ndi iwo osakhala mtundu wa anthu; ndidzautsa mkwiyo wao ndi mtundu wa anthu opusa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anandichititsa kukhala wansanje pamene ankapembedza chimene si mulungu ndi kundikwiyitsa chifukwa cha mafano awo achabechabe. Ine ndidzawachititsa kuti achite nsanje ndi mtundu wina wopandapake; ndidzawakwiyitsa ndi mtundu wina wachabechabe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Anautsa nsanje yanga ndi cinthu cosati Mulungu; Anautsa mkwiyo wanga om zopanda pace zao. Ndidzautsa nsanje yao ndi iwo osakhala mtundu wa anthu; Ndidzautsa mkwiyo wao ndi mtundu wa anthu opusa.