Deuteronomy 32:25 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
M'miseu adzafa chifukwa cha nkhondo, m'nyumba adzafa ndi mantha. Anyamata ndi atsikana adzafa, ngakhale ana ndi okalamba omwe sadzakhala ndi moyo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pabwalo lupanga lidzalanda, ndi m'zipinda mantha; lidzaononga mnyamata ndi namwali, woyamwa pamodzi ndi munthu waimvi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mʼmisewu lupanga lidzawasandutsa kukhala wopanda ana; mantha adzalamulira nyumba zawo. Anyamata ndi atsikana adzafa, ngakhalenso makanda ndi okalamba.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pabwalo lupanga lidzalanda, Ndi m'zipinda mantha; Lidzaononga mnyamata ndi namwali, Woyamwa pamodzi ndi munthu waimvi.