Deuteronomy 32:30 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nanga chifukwa chiyani munthu mmodzi adagonjetsa anthu chikwi chimodzi, ndipo anthu aŵiri adagonjetsa zikwi khumi? Nchifukwa chakuti Chauta, Mulungu wao, waŵasiya, Mulungu wao wamphamvu waŵataya.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mmodzi akadapirikitsa zikwi, awiri akadathawitsa zikwi khumi, akadapanda kuwagulitsa Thanthwe lao, akadapanda kuwapereka Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kodi munthu mmodzi akanathamangitsa bwanji anthu 1,000 kapena anthu awiri kuthamangitsa anthu 10,000, kuti awagonjetse, Thanthwe lawo likanapanda kuwagulitsa, Yehova akanapanda kuwataya?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mmodzi akadapitikitsa zikwi, Awiri akadathawitsa zikwi khumi, Akadapanda kuwagulitsa Thanthwelao, Akadapanda kuwapereka Yehova.