Deuteronomy 32:35 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kulipsira nkwanga, kubwezera zoyenerera nkwanganso, nthaŵi yoti agwe idzakwana. Tsiku la masoka ao layandikira, chiwonongeko chao chikudza mofulumira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kubwezera chilango nkwanga, kubwezera komwe, pa nyengo ya kuterereka phazi lao; pakuti tsiku la tsoka lao layandika, ndi zinthu zowakonzeratu zifulumira kudza.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kubwezera chilango nʼkwanga; ndidzawalanga ndine. Pa nthawi yake phazi lawo lidzaterera; tsiku lawo la masautso layandikira ndipo chiwonongeko chawo chikubwera pa iwo mofulumira.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kubwezera cilango nkwanga, kubwezera komwe, Pa nyengo ya kuterereka phazi lao; Pakuti tsiku la tsoka lao layandika, Ndi zinthu zowakonzeratu zifulomira kudza.