Deuteronomy 32:36 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta adzachitira anthu ake zolungama, adzachitira atumiki ake zachifundo, pamene adzaona kuti mphamvu zao zatha, ndipo kuti sipatsala anthu, kaya ndi akapolo kapena mfulu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Popeza Yehova adzaweruza anthu ake, nadzachitira nsoni anthu ake; pakuona Iye kuti mphamvu yao yatha, wosatsala womangika kapena waufulu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova adzaweruza anthu ake ndipo adzachitira atumiki ake chifundo pamene adzaona kuti mphamvu zawo zatha ndipo kuti palibe amene watsala, kapolo kapena mfulu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Popeza Yehova adzaweruza anthuace, Nadzacitira nsoni anthu ace; Pakuona iye kuti mphamvu yao yatha, Wosatsala womangika kapena waufulu,