Deuteronomy 32:39 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Muwone tsopano kuti Mulungu uja ndine, Ine ndekha, palibenso mulungu wina. Ndimapha, Ine ndemwe ndimapatsanso moyo, ndimapweteka, Ine ndemwe ndimachiritsanso, ndipo palibe ndi mmodzi yemwe amene angathe kupulumutsa munthu m'manja mwanga.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tapenyani tsopano kuti Ine ndine Iye, ndipo palibe mulungu koma Ine; ndipha Ine, ndikhalitsanso ndi moyo, ndikantha, ndichizanso Ine; ndipo palibe wakulanditsa m'dzanja langa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Onani tsopano kuti Ine ndine Iyeyo! Palibe mulungu wina koma Ine ndekha. Ine ndimapha ndiponso kupereka moyo, ndavulaza ndipo ndidzachiritsa, ndipo palibe angathe kupulumutsa munthu mʼmanja mwanga.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tapenyani tsopano kuti Ine ndine iye, Ndipo palibe mulungu koma Ine; Ndipha Ine, ndikhalitsanso ndi mayo: Ndikantha, ndicizanso Ine; Ndipo palibe wakulanditsa m'dzanja langa.