Deuteronomy 32:41 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
kuti ndidzanola lupanga langa lochezimira, ndipo ndidzaona kuti chilungamo chichitike. Adani anga ndidzaŵabwezera chilango, amene amadana nane ndidzaŵalanga.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndikanola lupanga langa lonyezimira, ndi dzanja langa likagwira chiweruzo; ndidzabwezera chilango ondiukira, ndi kulanga ondida.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
pamene ndidzanola lupanga langa lonyezimira ndipo dzanja liligwira pakubweretsa chiweruzo, ndidzabwezera chilango adani anga ndi kulanga onse odana nane.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndikanola lupanga langa lonyezimira, Ndi dzanja langa likagwira ciweruzo; Ndidzabwezera cilango ondiukira, Ndi kulanga ondida.