Deuteronomy 32:43 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Inu mitundu yonse ya anthu, tamandani anthu a Chauta. Chauta amalanga onse opha anthu ake, amalipsira adani ake, ndipo amachotsa tchimo m'dziko la anthu ake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kondwerani, amitundu inu, ndi anthu ake; adzalipsira mwazi wa atumiki ake, adzabwezera chilango akumuukira, nadzafafanizira zoipa dziko lake, ndi anthu ake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kondwerani, inu mitundu yonse ya anthu pamodzi ndi anthu ake, pakuti Iye adzabwezera chilango anthu amene anapha atumiki ake; adzabwezera chilango adani ake ndipo adzakhululukira dziko lake ndi la anthu ake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kondwerani, amitundu inu, ndi anthu ace; Adzalipsira mwazi wa atumiki ace, Adzabwezera cilango akumuukira, Nadzafafanizira zoipa dziko lace, ndi anthu ace.