Deuteronomy 32:47 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mauŵa sikuti ndi mau achabe. Mau ameneŵa ndiwo moyo wanu. Muŵamvere, ndipo mudzakhalitsa m'dziko mukukakhalamolo uko kutsidya kwa Yordani.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti sichikhala kwa inu chinthu chopanda pake, popeza ndicho moyo wanu, ndipo mwa chinthu ichi mudzachulukitsa masiku anu m'dziko limene muolokera Yordani, kulilandira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mawuwa sikuti ndi mawu achabe kwa inu. Mawuwa ndi moyo wanu. Mukawamvera mudzakhala ndi moyo wautali mʼdziko limene mukukalitenga kukhala lanu mukawoloka Yorodani.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti sicikhala kwa inu cinthu copanda pace, popeza ndico moyo wanu, ndipo mwa cinthu ici mudzacurukitsa masiku anu m'dziko limene muolokera Yordano, kulilandira.