Deuteronomy 32:51 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chifukwa chake nchakuti inu nonse aŵiri simudakhulupirike kwa Ine pamaso pa Aisraele. Pamene munali ku madzi a Meriba, pafupi ndi mudzi wa Kadesi, m'chipululu cha Zini, simudandilemekeze kokwanira pamaso pa Aisraele.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
popeza munandilakwira pakati pa ana a Israele ku madzi a Meriba wa Kadesi m'chipululu cha Zini, popeza simunandipatula Ine pakati pa ana a Israele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chifukwa chake nʼchakuti inu nonse awiri simunakhulupirike kwa Ine pamaso pa Aisraeli pa madzi a Meriba ku Kadesi mʼchipululu cha Zini chifukwa simunandilemekeze kokwanira pakati pa Aisraeli.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
popeza munandilakwira pakati pa ana a Israyeli ku madzi a Meriba wa Kadesi m'cipululu ca Zini, popeza simunandipatula Ine pakati pa ana a Israyeli,