Deuteronomy 33:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Inu Chauta, thandizani fuko lao kuti likhale lamphamvu, zochita zao zikukondwetseni. Otsutsana nawo ndi odana nawo onse muŵaononge, kotero kuti asadzadzukenso.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Dalitsani, Yehova, mphamvu yake, nimulandire ntchito ya manja ake; akantheni m'chuuno iwo akumuukira, ndi iwo akumuda, kuti asaukenso.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Inu Yehova, dalitsani luso lake lonse ndipo mukondwere ndi ntchito za manja ake. Menyani adani awo mʼchiwuno kanthani amene amuwukira kuti asadzukenso.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Dalitsani, Yehova, mphamvu yace, Nimulandire nchito ya manja ace; Akantheni m'cuuno iwo akumuukira, Ndi iwo akumuda, kuti asaukenso.