Deuteronomy 33:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Dziko lao likhale ndi dzinthu dzopambana, lidalitsidwe ndi zokoma za Chauta amene adalankhula m'chitsamba choyaka chija. Madalitso onseŵa atsikire fuko la Yosefe, popeza kuti anali mtsogoleri pakati pa abale ake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndi zinthu zofunikatu za dziko lapansi, ndi kudzala kwake, ndi chivomerezo cha Iye anakhala m'chitsambayo. Mdalitso ufike pa mutu wa Yosefe, ndi pakati pa mutu wake wa iye wokhala padera ndi abale ake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
ndi mphatso zabwino kwambiri zochokera pa dziko lapansi ndi zonse zimene zili mʼmenemo ndiponso kukoma mtima kwa Iye amene amakhala mʼchitsamba choyaka moto. Madalitso onsewa akhale pa mutu pa Yosefe, wapaderadera pakati pa abale ake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi zinthu zofunikatu za dziko lapansi, ndi kudzala kwace, Ndi cibvomerezo ca iye anakhala m'citsambayo; Mdalitso ufike pa mutu wa Yosefe, Ndi pakati pa mutu wace wa iye wokhala padera ndi abale ace.