Deuteronomy 33:17 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yosefe ali ndi mphamvu zonga za ng'ombe yamphongo, nyanga zake ndi zonga za njati, adzapirikitsa anthu a mitundu ina ndi nyanga zimenezi. Onsewo adzaŵapirikitsira ku malekezero a dziko. Nyanga zimenezi ndi anthu zikwi khumi za Efuremu ndipo anthu zikwi za Manase.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Woyamba kubadwa wa ng'ombe yake, ulemerero ndi wake; nyanga zake ndizo nyanga zanjati; adzatunga nazo mitundu ya anthu pamodzi, kufikira malekezero a dziko lapansi. Iwo ndiwo zikwi khumi za Efuremu, iwo ndiwo zikwi za Manase.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ulemerero wake uli ngati ngʼombe yayimuna yoyamba kubadwa; nyanga zake zili ngati za njati. Ndi nyanga zakezo adzapirikitsa anthu a mitundu ina, ngakhale iwo amene akukhala ku malekezero a dziko lapansi. Nyanga zimenezi ndiye anthu miyandamiyanda a Efereimu; nyanga zimenezi ndiye anthu 1,000 a Manase.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Woyamba kubadwa wa ng'ombe yace, ulemerero ndi wace; Nyanga zace ndizo nyanga zanjati; Adzatunga nazo mitundu ya anthu pamodzi, kufikira malekezero a dziko lapansi. Iwo ndiwo zikwi khumi za Efraimu, Iwo ndiwo zikwi za Manase.