Deuteronomy 33:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Poŵadalitsapo adanena mau akuti, “Chauta adabwera kuchokera ku phiri la Sinai, natitulukira kuchokera ku Seiri, ndipo adatiŵalira kuchokera ku phiri la Parani. Angelo zikwi khumi anali naye pamodzi, moto woyaka unali m'manja mwake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anati, Yehova anafuma ku Sinai, nawatulukira ku Seiri; anaoneka wowala pa phiri la Parani, anafumira kwa opatulika zikwizikwi; ku dzanja lamanja lake kudawakhalira lamulo lamoto.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anati: “Yehova anabwera kuchokera ku Sinai ndipo anatulukira kuchokera ku Seiri; anawala kuchokera pa Phiri la Parani. Iye anabwera ndi chiwunyinji cha angelo kuchokera kummwera, moto woyaka uli mʼdzanja mwake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anati, Yehova anafuma ku Sinai, Nawaturukiraku Seiri; Anaoneka wowala pa phiri la Parana, Anafumira kwa opatulika zikwi zikwi; Ku dzanja lamanja lace kudawakhalira lamulo lamoto.