Deuteronomy 33:21 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adadzitengera dziko labwino kuti likhale lao, gawo la mtsogoleri lidaperekedwa kwa iwowo. Adasunga maweruzo ndi malamulo a Chauta pamene atsogoleri a Aisraele adasonkhanitsidwa pamodzi.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anadzisankhira gawo loyamba, popeza kumeneko kudasungika gawo la wolamulira; ndipo anadza ndi mafumu a anthu, anachita chilungamo cha Yehova, ndi maweruzo ake ndi Israele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anadzisankhira dziko labwino kwambiri; gawo la mtsogoleri anasungira iye. Pamene atsogoleri a anthu anasonkhana, anachita chifuniro cha Yehova molungama, ndiponso malamulo onena za Israeli.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anadzisankhira gawo loyamba, Popeza kumeneko kudasungika gawo la wolamulira; Ndipo anadza ndi mafumu a anthu, Anacita cilungamo ca Yehova, Ndi maweruzo ace ndi Israyeli.