Deuteronomy 33:23 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Za fuko la Nafutali, adati, “Chauta wakomera mtima Nafutali namdalitsa kwambiri. Dziko lake lifika mpaka kumwera kuchokera ku nyanja ya Galileya.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Za Nafutali anati, Nafutali, wokhuta nazo zomkondweretsa, wodzala ndi mdalitso wa Yehova; landira kumadzulo ndi kumwera.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Za fuko la Nafutali anati: “Nafutali wadzaza ndi kukoma mtima kwa Yehova ndipo ndi wodzaza ndi madalitso ake; cholowa chake chidzakhala mbali ya kummwera kwa nyanja.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Za Nafitali anati, Nafitali, wokhuta nazo zomkondweretsa, Wodzala ndi mdalitso wa Yehova; Landira kumadzulo ndi kumwela.