Deuteronomy 33:27 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta ndiye amene ali kothaŵirako ndipo pa dziko lapansili amakusungani ndi mphamvu zosatha. Adathaŵitsa adani anu onse pamene munkayenda, ndipo adakuuzani kuti muŵaononge onse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mulungu wamuyaya ndiye mokhaliramo mwako; ndi pansipo pali manja osatha. Ndipo aingitsa mdani pamaso pako, nati, Ononga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mulungu wamuyaya ndiye pothawirapo pathu, ndipo pa dziko lapansi amakusungani ndi mphamvu zosatha. Adzathamangitsa patsogolo panu mdani wanu, adzanena kuti, ‘Muwonongeni!’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mulungu wamuyaya ndiye mokhaliramo mwako; Ndi pansipo pali manja osatha. Ndipo aingitsa mdani pamaso pako, Nati, Ononga.