Deuteronomy 33:29 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iwe Israele, ndiwetu wodala, wofanafana nawe palibe. Ndiwe mtundu umene Chauta adaupulumutsa. Chauta weniweniyo ndiye chishango chako ndi lupanga lako, ndiye amene amakutchinjiriza ndi kukupambanitsa. Adani ako adzafika kudzapempha kuti uŵachitire chifundo, koma iwe udzaŵapondereza pansi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Wodala iwe, Israele; akunga iwe ndani, mtundu wa anthu opulumutsidwa ndi Yehova, ndiye chikopa cha thandizo lako, Iye amene akhala lupanga la ukulu wako! Ndi adani ako adzakugonjera; ndipo udzaponda pa misanje yao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwe Israeli, ndiwe wodala! Wofanana nanu ndani anthu opulumutsidwa ndi Yehova? Iye ndiye chishango ndi mthandizi wanu ndi lupanga lanu la ulemerero. Adani ako adzakugonjera, ndipo iwe udzapondereza pansi malo awo achipembedzo.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Wodala iwe, Israyeli; Akunga iwe ndani, mtundu wa anthu opulumutsidwa ndi Yehova, Ndiye cikopa ca thandizo lako, Iye amene akhala lupanga la ukulu wako! Ndi adani ako adzakugonjera; Ndipo udzaponda pa misanje yao.