Deuteronomy 33:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Za fuko la Yuda, adati, “Inu Chauta, mverani pamene iwo akulira, athandizeni, ndipo muŵalumikizenso ndi mafuko ena. Inu Chauta, muŵalimbikitse kuti adziteteze okha, ndipo muŵathandize polimbana ndi adani ao.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Za Yuda ndi izi; ndipo anati, Imvani, Yehova, mau a Yuda, ndipo mumfikitse kwa anthu ake; manja ake amfikire; ndipo mukhale inu thandizo lake pa iwo akumuukira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo ponena za Yuda anati: “Inu Yehova, imvani kulira kwa Yuda; mubweretseni kwa anthu ake. Ndi manja ake omwe adziteteze yekha. Inu khalani thandizo lake polimbana ndi adani ake!”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Za Yuda ndi izi; ndipo anati, Imvani, Yehova, mau a Yuda, Ndipo mumfikitse kwa anthu ace; Manja ace amfikire; Ndipo mukhale inu thandizo lace pa iwo akumuukira.