Deuteronomy 33:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iwo adaonetsa kuti ankakhulupirira Inu kupambana makolo ao, abale ao kapenanso ana ao. Adamvera malamulo anu, ndipo adakhulupirika pa chipangano chanu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
amene anati za atate wake ndi amai wake, sindinamuone; Sanazindikire abale ake, sanadziwe ana ake omwe; popeza anasamalira mau anu, nasunga chipangano chanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye ananena za abambo ake ndi amayi ake kuti, ‘Sindilabadira za iwo.’ Sanasamale za abale ake kapena ana ake, koma anayangʼanira mawu anu ndipo anateteza pangano lanu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Amene anati za atate wace ndi amai wace, Sindinamuone; Sanazindikira abale ace, Sanadziwa ana ace omwe; Popeza anasamalira mau anu, Nasunga cipangano canu.