Deuteronomy 34:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mose adakwera phiri la Nebo kuchokera ku zigwa za Mowabu. Adakafika mpaka pamwamba pa phiri la Pisiga kuvuma kwa Yeriko. Ndipo kumeneko Chauta adamuwonetsa dziko lonse, dziko la Giliyadi mpaka ku dziko la Dani.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Mose anakwera kuchokera ku zidikha za Mowabu, kunka kuphiri la Nebo, pamwamba pa Pisiga, popenyana ndi Yeriko. Ndipo Yehova anamuonetsa dziko lonse la Giliyadi, kufikira ku Dani;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo Mose anakwera Phiri la Nebo kuchokera ku chigwa cha Mowabu ndi kukafika pamwamba pa Phiri la Pisiga, kummawa kwa Yeriko. Kumeneko Yehova anamuonetsa dziko lonse; kuchokera ku Giliyadi mpaka ku Dani.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Mose anakwera kucokera ku zidikha za Moabu, kumka ku phiri la Nebo, pamwamba pa Pisiga, popenyana ndi Yeriko. Ndipo Yehova anamuonetsa dziko lonse la Gileadi, kufikira ku Dani;