Deuteronomy 34:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Palibe mneneri wina aliyense amene adachitapo zozizwitsa ndi zodabwitsa monga zimene Chauta adauza Mose kuti achite pamaso pa mfumu ya ku Ejipito, ndi pa akulu ake, ndi m'dziko lake lonse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
kunena za zizindikiro ndi zozizwa zonse zimene Yehova anamtumiza kuzichita m'dziko la Ejipito kwa Farao, ndi anyamata ake onse, ndi dziko lake lonse;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Amene anachita zizindikiro zozizwitsa zonsezi ndi zozizwitsa zimene Yehova anamutuma kuti achite mu Igupto, kwa Farao ndi kwa nduna zake zonse ndiponso mʼdziko lake lonse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
kunena za zizindikilo ndi zozizwa zonse zimene Yehova anamtumiza kuzicita m'dziko la Aigupto kwa Farao, ndi anyamata ace onse, ndi dziko lace lonse;