Deuteronomy 34:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Chauta adauza Mose kuti, “Ilo ndilo dziko limene lija ndidalonjeza Abrahamu, Isaki ndi Yakobe, kuti ndidzapatsa zidzukulu zao. Ndakulola kuti uliwone, koma kuloŵamo kokha sindikulola.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yehova anati kwa iye, Si ili dziko ndinalumbirira Abrahamu, Isaki ndi Yakobo, ndi kuti, Ndidzalipereka kwa mbeu zako. Ndinakuonetsa ili m'maso, koma sudzaolokako.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka Yehova anawuza Mose kuti, “Limenelo ndi dziko limene ndinalonjeza mwa lumbiro kwa Abrahamu, Isake ndi Yakobo pamene ndinanena kuti, ‘Ndidzalipereka kwa zidzukulu zanu.’ Ndakulola kuti ulione, koma sudzawoloka kuti ukalowemo.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yehova anati kwa iye, Si ili dziko ndinalumbirira Abrahamu, Isake, ndi Yakobo, ndi kuti, Ndidzalipereka kwa mbeu zako. Ndinakuonetsa ili m'maso, koma sudzaolokako.