Deuteronomy 34:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta adamuika ku Mowabu komweko m'chigwa, moyang'anana ndi mudzi wa Betepeori. Koma palibe ndi mmodzi yemwe amene akudziŵa malo enieni a mandawo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Iye anamuika m'chigwa m'dziko la Mowabu popenyana ndi Betepeori; koma palibe munthu wakudziwa kumanda kwake kufikira lero lino.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova anamuyika mʼmanda ku Mowabu, mʼchigwa choyangʼanana ndi Beti-Peori, koma mpaka lero palibe amene amadziwa pamene pali manda ake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo iye anamuika m'cigwa m'dziko la Moabu popenyana ndi Beti-peori; koma palibe munthu wakudziwa kumanda kwace kufikira lero lino.