Deuteronomy 4:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsopano inu Aisraele, muzimvera malamulo ndi malangizo onse amene ndikukuphunzitsani, kuti mukhale ndi moyo. Ndipo mudzaloŵa ndi kukhazikika m'dziko limene Chauta, Mulungu wa makolo anu, akukupatsani.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo tsopano, Israele, tamverani malemba ndi maweruzo, amene ndikuphunzitsani muwachite; kuti mukhale ndi moyo, ndi kulowa, ndi kulandira dziko limene Yehova Mulungu wa makolo anu akupatsani.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mverani inu Aisraeli, malangizo ndi malamulo amene ndikuphunzitseni. Muwatsatire kuti mukhale ndi moyo ndi kuti mulowe ndi kutenga dziko limene Yehova Mulungu wa makolo anu akukupatsani.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo tsopano, Israyeli, dioloketu tamverani malemba ndi maweruzo, amene ndikuphunzitsani muwacite; kuti mukhale ndi moyo, ndi kulowa, ndi kulandira dziko limene Yehova Mulungu wa makolo anu akupatsani.