Deuteronomy 4:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Muziŵauza za tsiku lija pamene mudaima pamaso pa Chauta, Mulungu wanu, ku phiri la Horebu kuja. Kumeneko Chauta adandiwuza kuti, “Asonkhanitseni anthu. Ndifuna kuti iwo amve zimene ndilankhule, kuti aphunzire kundiwopa nthaŵi zonse adzakhale ndi moyo pa dziko lapansi, kenaka azidzaphunzitsanso ana ao kundimvera.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tsikuli munaima pamaso pa Yehova Mulungu wanu m'Horebu muja Yehova anati kwa ine, Ndisonkhanitsire anthu, ndidzawamvetsa mau anga, kuti aphunzire kundiopa Ine masiku ao onse akukhala ndi moyo pa dziko lapansi, ndi kuti aphunzitse ana ao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kumbukirani tsiku limene munayimirira pamaso pa Yehova Mulungu wanu ku Horebu, pamene anati kwa ine, “Sonkhanitsa anthu pamaso panga kuti amve mawu anga ndi kuti aphunzire kundilemekeza mʼmoyo wawo onse mʼdzikomo ndi kuti ana awo aziwaphunzitsa zimenezi.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tsikuli munaima pamaso pa Yehova Mulungu wanu m'Horebe muja Yehova anati kwa ine, Ndisonkhanitsire anthu, ndidzawamvetsa mau anga, kuti aphunzire kundiopa Ine masiku ao onse akukhala ndi moyo pa dziko lapansi, ndi kuti aphunzitse ana ao.