Deuteronomy 4:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Inu mudadza, mudaima patsinde pa phiri. Phirilo linkayaka moto mokwera mpaka ku thambo, ndipo linali lophimbidwa ndi chiwutsi chabii ndi chimdima.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo munayandikiza ndi kuima patsinde pa phiri; ndi phirilo linayaka moto kufikira pakati pa thambo; kunali mdima, ndi mtambo, inde mdima bii.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Munabwera pafupi ndi kuyima pa tsinde pa phiri pamene phirilo limayaka moto umene umafika mpaka kumwamba. Panalinso mtambo wakuda ndi mdima wambiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo munayandikiza ndi kuima patsinde pa phiri; ndi phizilo linayaka mota kufikira pakati pa thambo; kunali mdima, ndi mtambo, inde mdima bii.