Deuteronomy 4:20 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma inu ndinu anthu amene Mulungu adakutulutsani ku dziko la Ejipito, ng'anjo yotentha ija. Adakutulutsanimo kuti mukhale anthu akeake monga m'mene muliri leromu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Yehova anakutengani, nakutulutsani m'ng'anjo yamoto, m'Ejipito, mukhale kwa Iye anthu a cholowa chake, monga mukhala lero lino.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma inuyo, Yehova anakutengani ndi kukutulutsani mʼngʼanjo yosungunulira zitsulo, ku Igupto kuti mukhale anthu olandira chuma chake monga mmene mulili tsopano.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma Yehova anakutengani, nakuturutsani m'ng'anjo yamoto, m'Aigupto, mukhale kwa iye anthu a colowa cace, monga mukhala lero lino.