Deuteronomy 4:25 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ngakhale mutakhala m'dzikomo nthaŵi yaitali, ndi kubereka ana ndi zidzukulu, musadzachimwe pakudzipangira fano la maonekedwe ena aliwonse. Pamaso pa Chauta ndi zoipa zimenezi, ndipo adzapsa nazo mtima.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mutakabala ana, ndi zidzukulu, ndipo mutakakhala nthawi yaikulu m'dzikomo, ndi kudziipsa, ndi kupanga fano losema, m'chifaniziro cha kanthu kalikonse, ndi kuchita choipa pamaso pa Yehova, kuutsa mkwiyo wake:
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mukadzakhala nthawi yayitali mʼdzikomo ndi kubereka ana ndi kukhala ndi zidzukulu ndipo mukadzasokonekera ndi kupanga fano la mtundu uliwonse, nʼkumachita zoyipa pamaso pa Yehova Mulungu wanu ndi kumukwiyitsa,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mutakabala ana, ndi zidzukulu, ndipo mutakakhala nthawi yaikuru m'dzikomo, ndi kudziipsa, ndi kupanga fano losema, m'cifaniziro ca kanthu kali konse, ndi kucita coipa pamaso pa Yehova, kuutsa mkwiyo wace: