Deuteronomy 4:28 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kumeneko muzidzatumikira milungu yopanga ndi manja, monga yamtengo ndi yamwala, milungu imene singathe kupenya kapena kumva, kudya kapenanso kununkhiza.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kumeneko mudzatumikira milungu, ntchito ya manja a anthu, mtengo ndi mwala, yosapenya, kapena kumva, kapena kudya, kapena kununkhiza.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kumeneko mudzapembedza milungu ya mitengo ndi miyala yopangidwa ndi anthu, imene singaone kapena kumva kapena kudya kapena kununkhiza.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kumeneko mudzatumikira milungu, nchito ya manja a anthu, mtengo ndi mwala, yosapenya, kapena kumva, kapena kudya, kapena kununkhiza.