Deuteronomy 4:31 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Paja Chauta, Mulungu wanu, ndi Mulungu wachifundo. Sadzakulekererani kapena kukuwonongani. Chipangano chimene Iye adachita molumbira ndi makolo anu, sadzachiiŵala.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
popeza Yehova Mulungu wanu ndiye Mulungu wachifundo; sadzakusiyani, kapena kukuonongani, kapena kuiwala chipangano cha makolo anu chimene analumbirira iwo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti Yehova Mulungu wanu ndi Mulungu wachifundo, Iye sadzakutayani kapena kukuwonongani kapena kuyiwala pangano lake ndi makolo anu, limene analitsimikiza mwa lumbiro.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
popeza Yehova Mulungu wanu ndiye Mulungu wacifundo; sadzakusiyani, kapena kukuonongani, kapena kuiwala cipangano ca makolo anu cimene analumbirira iwo.