Deuteronomy 4:32 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tafufuzani zakale, inu musanabadwe, kuyambira pa tsiku lija limene Mulungu adalenga munthu pa dziko lapansi. Tafufuzani pa dziko lonse lapansi. Kodi chachikulu chonga chimenechi chidachitikapo ndi kale lonse? Kodi alipo wina amene adamvapo zotere?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti, funsiranitu, masiku adapitawo, musanakhale inu, kuyambira tsikuli Mulungu analenga munthu pa dziko lapansi, ndi kuyambira malekezero ena a thambo kufikira malekezero anzake a thambo, ngati chinthu chachikulu chonga ichi chinamveka, kapena kuchitika?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsopano tafunsani za masiku a mʼmbuyomu, zakale inu musanabadwe, kuyambira tsiku limene Mulungu analenga munthu pa dziko lapansi. Tafufuzani kuyambira kumapeto mpaka mapeto anzake a thambo. Kodi chinachitikako china chachikulu ngati ichi, kapena chinayamba chamvekako chokhala ngati ichi?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti, funsiranitu, masiku adapitawo, musanakhale inu, kuyambira tsikuli Mulungu analenga munthu pa dziko lapansi, ndi kuyambira malekezero ena a thambo kufikira malekezero anzace a thambo, ngati cinthu cacikuru conga ici cinamveka, kapena kucitika?