Deuteronomy 4:34 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kodi alipo mulungu wina aliyense amene adaapita kukadzitengera anthu kuŵachotsa pakati pa fuko lina, naŵasandutsa anthu akeake, monga muja Chauta, Mulungu wanu, adakuchitirani inu ku Ejipito kuja? Iye adachita zimenezo ndi mphamvu zake zazikulu, inu mukupenya. Adadzetsa miliri pamodzi ndi nkhondo, adachita zozizwitsa ndi zodabwitsa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kapena kodi anayesa Mulungu kumuka ndi kudzitengera mtundu mwa mtundu wina wa anthu, ndi mayesero, ndi zizindikiro, ndi zozizwa, ndi nkhondo, ndi mwa dzanja lamphamvu, ndi mkono wotambasuka, ndi mwa zoopsa zachikulu, monga mwa zonse Yehova Mulungu wanu anakuchitirani m'Ejipito pamaso panu?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kodi alipo mulungu amene anayeserapo kudzitengera mtundu wa anthu kuwachotsa mu mtundu unzake mwa mayesero, zizindikiro zozizwitsa, nkhondo, komanso mwa mphamvu zake zopanda malire, kapena mwa zochita zazikulu ndi zochititsa mantha, monga zimene Yehova Mulungu wanu anakuchitirani ku Igupto inu mukupenya?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kapena kodi anayesa Mulungu kumuka ndi kudzitengera mtundu mwa mtundu wina wa anthu, ndi mayesero, ndi zizindikilo, ndi zozizwa, ndi nkhondo, ndi mwa dzanja lamphamvu, ndi mkono wotambasuka, ndi mwa zoopsa zazikuru, monga mwa zonse Yehova Mulungu wanu anakucitirani m'Aigupto pamaso panu?