Deuteronomy 4:36 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta adalola kuti mumve mau ake kuchokera kumwamba, kuti pakutero akuphunzitseni. Pa dziko lapansi pano Chauta adakuwonetsani moto waukulu, ndipo mudamva akulankhula nanu kuchokera m'motomo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Anakumvetsani mau ake kuchokera kumwamba, kuti akuphunzitseni; ndipo pa dziko lapansi anakuonetsani moto wake waukulu; nimunamva mau ake pakati pa moto.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kuchokera kumwamba, Iye anafuna kuti inu mumve mawu ake ndi kuti mukhale osunga mwambo. Pa dziko lapansi anakuonetsani moto waukulu, ndipo inu munamva mawu ake kuchokera mʼmotomo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Anakumvetsani mau ace kucokera kumwamba, kuti akuphunzitseni; ndipo pa dziko lapansi anakuonetsani moto wace waukuru; nimunamva mau ace pakati pa moto.