Deuteronomy 4:40 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Muzimvera malangizo ndi malamulo ake onse amene ndakupatsani leroŵa. Mukatero, zinthu zidzakuyenderani bwino inuyo ndi zidzukulu zanu, ndipo mudzakhalitsa m'dziko limene Chauta, Mulungu wanu, adzakupatsani kuti likhale lanu mpaka muyaya.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Muzisunga malemba ake, ndi malamulo ake, amene ndikuuzani lero lino, kuti chikukomereni inu ndi ana anu akukutsatani, ndi kuti masiku anu achuluke pa dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani likhale lanu kosatha.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Sungani malangizo ake ndi malamulo ake amene ndikukupatsani lero lino, kuti zikuyendereni bwino inu ndi ana anu kutsogoloko, ndi kuti mukhalitse mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani kwa nthawi zonse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Muzisunga malemba ace, ndi malamulo ace, amene ndikuzuzani lero lino, kuti cikukomereni inu ndi ana anu akukutsatani, ndi kuti masiku anu acuruke pa dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani likhale lanu kosatha.