Deuteronomy 4:42 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
kumene munthu wopha mnzake mwangozi, osati mwachidani, ankatha kuthaŵirako ndi kupulumutsa moyo wake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
kuti athawireko wakupha munthu, osamupha mnansi wake dala, osamkwiyira ndi kale lonse; ndi kuti, akathawira ku umodzi wa midzi iyi, akhale ndi moyo:
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
kumene aliyense amene wapha munthu akhoza kuthawirako ngati wopha munthuyo sanaphe mnzakeyo mwadala ndi maganizo oyipa. Iye akhoza kuthawira ku umodzi mwa mizinda imeneyi napulumutsa moyo wake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
kuti athawireko wakupha munthu, osamupha mnansi wace dala, osamkwiyira ndi kale lonse; ndi kuti, akathawira ku umodzi wa midzi iyi, akhale ndi moyo: