Deuteronomy 4:43 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
A fuko la Rubeni, mzinda wao unali Bezeri umene unali m'chipululu, m'dziko lamapiri. A fuko la Gadi, mzinda wao unali Ramoti umene unali m'dziko la Giliyadi. Ndipo a fuko la Manase mzinda wao unali Golani umene unali m'dziko la Basani.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndiyo Bezeri, m'chipululu, m'dziko lachidikha, ndiwo wa Arubeni; ndi Ramoti m'Giliyadi, ndiwo wa Agadi; ndi Golani, m'Basani, ndiwo wa Amanase.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mizindayo inali iyi: ku fuko la Rubeni, unali mzinda wa Bezeri ku mapiri a ku chipululu; ku fuko la Gadi, unali Ramoti ku Giliyadi; ndipo ku fuko la Manase, unali Golani ku Basani.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndiyo Bezere, m'cipululu, m'dziko lacidikha, ndiwo wa Anrubeni; ndi Ramoti m'Gileadi, ndiwo wa Agadi; ndi Golani, m'Basana, ndiwo wa Amanase.