Deuteronomy 4:46 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Aisraelewo anali m'chigwa kuvuma kwa mtsinje wa Yordani, kuyang'anana ndi mudzi wa Betepeori. Kumeneko ndi dziko la Sihoni, mfumu ya Aamori, amene ankalamula mzinda wa Hesiboni, ndipo Mose ndi Aisraelewo atatuluka m'dziko la Ejipito, adamgonjetsa Sihoniyo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
tsidya lija la Yordani, m'chigwa cha pandunji pa Betepeori, m'dziko la Sihoni mfumu ya Aamori, wakukhala m'Hesiboni, amene Mose ndi ana a Israele anamkantha, potuluka iwo m'Ejipito;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anali ku chigwa cha kufupi ndi Beti-Peori mbali ya kummawa kwa Yorodani, mʼdziko la Sihoni mfumu ya Aamori amene ankalamulira ku Hesiboni ndipo anagonjetsedwa ndi Mose ndi Aisraeli pamene ankachokera ku Igupto.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
tsidya lija la Yordano, m'cigwa ca pandunji pa Beti Peori, m'dziko la Sihoni mfumu ya Aamori, wakukhala m'Hesiboni, amene Mose ndi ana a Israyeli anamkantha, poturuka iwo m'Aigupto;