Deuteronomy 4:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndakuphunzitsani malamulo ndi malangizo onse, monga momwe Chauta, Mulungu wanga, adandilamulira. M'dziko limene mudzaloŵa ndi kukhalamolo, muzikamvera malamulo ameneŵa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Taonani, ndinakuphunzitsani malemba ndi maweruzo, monga Yehova Mulungu wanga anandiuza ine, kuti muzichita chotero pakati pa dziko limene mumkako kulilandira likhale lanulanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Taonani, ndakuphunzitsani malangizo ndi malamulo monga Yehova Mulungu wanga anandilamulira kuti inuyo muwatsatire mʼdziko limene mukulowa ndi kulitengali.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Taonani, ndinakuphunzitsani malemba ndi maweruzo, monga Yehova Mulungu wanga anandiuza ine, kuti muzicita cotero pakati pa dziko limene mumkako kulilandira likhale lanu Lanu.