Deuteronomy 4:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mukaŵasunge ndi kuŵatsata, ndipo chimenechi chidzaonetsa anthu a mitundu ina kuti ndinu anthu anzeru ndi omvetsa zinthu bwino. Akadzamva malamulo onseŵa, iwowo adzati, “Mtundu umenewu ndi waukulu, wanzeru ndi womvetsa zinthu bwino.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake asungeni, achiteni; pakuti ichi ndi nzeru zanu ndi chidziwitso chanu pamaso pa mitundu ya anthu akumva malemba ndi kuti, Ndithu mtundu waukulu uwu, ndiwo athu anzeru ndi akuzindikira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Muwasunge mosamalitsa pakuti zimenezi zidzaonetsa nzeru zanu ndi kuzindikira kwanu kwa anthu a mitundu ina, amene adzamva za malangizo onsewa nati, “Ndithudi, mtundu waukulu uwu ndi wa anthu anzeru ndi ozindikira.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace asungeni, aciteni; pakuti ici ndi nzeru zanu ndi cidziwitso canu pamaso pa mitundu ya anthu akumva malemba ndi kuti, Ndithu mtundu waukuru uwu, ndiwo anthu anzeru ndi akuzindikira.