Deuteronomy 4:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Palibe mtundu wina uliwonse kaya ndi waukulu chotani, umene uli ndi malamulo ndi malangizo achilungamo onga aŵa amene ndakupatsani leroŵa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mtundu waukulu wa anthu ndi uti, wakukhala nao malemba ndi maweruzo olungama, akunga chilamulo ichi chonse ndichiika pamaso panu lero lino?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo ndi mtundu uti mwa mitundu ya anthu umene ndi waukulu chotere kuti nʼkukhala ndi malangizo ndi malamulo olungama ngati malamulo amene ndikuyika pamaso panu lero?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mtundu waukuru wa anthu ndi uti, wakukhala nao malemba ndi maweruzo olungama, akunga cilamulo ici conse ndiciika pamaso panu lero lino?