Deuteronomy 4:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mukhale tcheru, ndipo musadzaiŵale zonse zimene mudaziwona. Zimenezo zisachoke m'mitima mwanu pa moyo wanu wonse. Muzizifotokoza kwa ana anu ndi kwa zidzukulu zanu zomwe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chokhachi, dzichenjerani nokha, ndi kusunga moyo wanu mwachangu, kuti mungaiwale zinthuzi adaziona maso anu, ndi kuti zisachoke kumtima kwanu masiku onse a moyo wanu; koma muzidziwitsa ana anu ndi zidzukulu zanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Inu mungosamala ndi kudziyangʼanira kwambiri nokha kuti musayiwale zimene maso anu aona. Musalole kuti zichoke mʼmitima mwanu pa moyo wanu wonse. Zimenezi muziphunzitse kwa ana anu ndi zidzukulu zanu ngakhale mʼtsogolo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cokhaci, dzicenjerani nokha, ndi kusunga moyo wanu mwacangu, kuti mungaiwale zinthuzi adaziona maso anu, ndi kuti zisacoke kumtima kwanu masiku onse a moyo wanu; koma muzidziwitsa ana anu ndi zidzukulu zanu.