Deuteronomy 5:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma tsiku lachisanu ndi chiŵiri ndi la Sabata la Chauta, Mulungu wako. Pa tsiku limenelo, usagwire ntchito iliyonse iweyo, mwana wako wamwamuna, mwana wako wamkazi, wantchito wako wamwamuna, mdzakazi wako, ng'ombe yako, bulu wako, kaya choŵeta chako chilichonse, ngakhale mlendo wokhala m'mudzi mwako. Motero atumiki ako aamuna ndi aakazi azipumanso monga iwe wemwe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
koma tsiku lachisanu ndi chiwiri ndilo Sabata la Yehova Mulungu wako; usamagwira ntchito iliyonse, iwe, kapena mwana wako wamwamuna, kapena mwana wako wamkazi, kapena wantchito wako wamwamuna, kapena wantchito wako wamkazi, kapena ng'ombe yako, kapena bulu wako, kapena zoweta zako zilizonse, kapena mlendo wokhala m'mudzi mwako; kuti wantchito wako wamwamuna ndi wantchito wako wamkazi apumule monga iwe mwini.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
koma tsiku lachisanu ndi chiwiri ndi Sabata, tsiku loperekedwa kwa Yehova Mulungu wako. Tsiku limeneli musagwire ntchito iliyonse, inuyo kapena mwana wanu wamwamuna kapena mwana wanu wamkazi kapena wantchito wanu wamwamuna kapena mdzakazi wanu kapena ngʼombe yanu kapena bulu wanu kapena ziweto zanu kapena mlendo amene akukhala mʼmudzi mwanu, motero ndiye kuti wantchito wanu wamwamuna ndi wantchito wanu wamkazi adzapumula monga inuyo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
koma tsiku lacisanu ndi ciwiri ndilo Sabata la Yehova Mulungu wako; usamagwira nchito iri yonse, iwe, kapena mwana wako wamwamuna, kapena mwana wako wamkazi, kapena wanchito wako wamwamuna, kapena wanchito wako wamkazi, kapena ng'ombe yako, kapena buru wako, kapena zoweta zako ziri zonse, kapena mlendo wokhala m'mudzi mwako; kuti wanchito wako wamwamuna ndi wanchito wako wamkazi apumule monga iwe mwini.