Deuteronomy 5:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Uzikumbukira kuti paja udaali kapolo m'dziko la Ejipito, ndipo kuti Ine Chauta, Mulungu wako, ndidakutulutsako ndi dzanja lamphamvu ndi mkono wotambasula. Nchifukwa chake Chauta, Mulungu wako, adakulamula kuti uzisunga tsiku la Sabata ndi kuliyeretsa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo uzikumbukira kuti unali kapolo m'dziko la Ejipito, ndi kuti Yehova Mulungu wako anakutulutsako ndi dzanja lamphamvu ndi mkono wotambasuka; chifukwa chake Yehova Mulungu wako anakulamulira kusunga tsiku la Sabata.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kumbukira kuti unali kapolo ku Igupto ndipo Yehova Mulungu wako anakutulutsa kumeneko ndi dzanja lamphamvu ndi lotambasuka. Choncho Yehova Mulungu wako akukulamula kuti uzisunga tsiku la Sabata.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo uzikumbukilakuti unali kapolo m'dziko la Aigupto, ndi kuti Yehova Mulungu wako anakuturutsako ndi dzanja lamphamvu ndi mkono wotambasuka; cifukwa cace Yehova Mulungu wako anakulamulira kusunga tsiku la Sabata.