Deuteronomy 5:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Uzilemekeza atate ako ndi amai ako, monga momwe Chauta, Mulungu wako, adakulamulira, kuti pakutero masiku a moyo wako achuluke ndipo kuti zinthu zikuyendere bwino m'dziko limene Chauta, Mulungu wako, akukupatsa iwe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Lemekeza atate wako ndi amai ako, monga Yehova Mulungu wako anakulamulira; kuti masiku ako achuluke, ndi kuti chikukomere, m'dziko limene Yehova Mulungu wako akupatsa iwe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Lemekeza abambo ako ndi amayi ako monga Yehova Mulungu wako wakulamulira iwe kuti ukhale ndi moyo wautali ndi kuti zikuyendere bwino mʼdziko limene Yehova Mulungu wako akukupatsa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Lemekeza atate wako ndi amako, monga Yehova Mulungu wako anakulamulira; kuti masiku ako acuruke, ndi kuti cikukomere, m'dziko limene Yehova Mulungu wako akupatsa iwe.