Deuteronomy 5:22 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta adaalankhula mau ameneŵa kwa inu nonse amene mudaasonkhana kuphiri kuja. Iye adanena mau ameneŵa osaonjezerapo kanthu, ndipo adalankhula mau amphamvu, kuchokera m'moto, m'mitambo ndiponso mu mdima wandiweyani. Pambuyo pake adalemba malamulo khumiwo pa miyala iŵiri, ndipo adandipatsa ine.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Yehova ananena mau awa kwa msonkhano wanu wonse, m'phirimo ali pakati pa moto, pamtambo, pamdima bii, ndi mau akulu; osaonjezapo kanthu. Ndipo anawalembera pa magome awiri amiyala, nandipatsa awa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Awa ndi malamulo amene Yehova anayankhula ndi mawu okweza kwa gulu lanu lonse pa phiri paja mʼmoto, mtambo ndi mdima woopsa, sanawonjezerepo kanthu. Ndipo anawalemba pa mapale awiri amiyala ndi kundipatsa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Yehova ananena mau awa kwa msonkhano wanu wonse, m'phirimo ali pakati pa moto, pamtambo, pamdima bii, ndi mau akuru; osaonjezapo kanthu. Ndipo anawalembera pa magome awiri amiyala, nandipatsa awa.