Deuteronomy 5:29 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ine ndikufuna kuti aziganiza zimenezo masiku onse. Ndikufuna kuti azindiwopa nthaŵi zonse, ndipo kuti azimvera malamulo anga, kuti zinthu ziŵayendere bwino iwowo ndi zidzukulu zao mpaka muyaya.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ha? Mwenzi akadakhala nao mtima wotere wakundiopa Ine, ndi kusunga malamulo anga masiku onse, kuti chiwakomere iwo ndi ana ao nthawi zonse!
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Zikanakhala bwino akanakhala ndi mtima wondiopa ndi kusunga malamulo anga nthawi zonse kuti zinthu ziziwayendera bwino, iwowo pamodzi ndi ana awo kwamuyaya.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ha! mwenzi akadakhala nao mtima wotere wakundiopa Ine, ndi kusunga malamulo anga masiku onse, kuti ciwakomere iwo ndi ana ao nthawi zonse!